1 Samuel 19:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atamva zimenezi Saulo adafunsa Mikala kuti, “Chifukwa chiyani wandinyenga chotere pa kulola kuti mdani wanga athaŵe?” Mikala adayankha kuti, “Davide adaandiwuza kuti, ‘Undilole ndipite. Ngati sutero, ndikupha.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Saulo kwa Mikala, Wandinyengeranji chomwechi, ndi kulola mdani wanga apulumuke? Ndipo Mikala anayankha Saulo, Iye anati kwa ine, Undilole ndipite, ndingakuphe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Sauli anafunsa Mikala kuti, “Nʼchifukwa chiyani wandinamiza chotere polola kuti mdani wanga athawe?” Mikala anayankha kuti, “Davide anandiwuza kuti, ‘Ukapanda kutero ndikupha.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Sauli kwa Mikala, Wandinyengeranii comweci, ndi kulola mdani wanga apulumuke? Ndipo Mikala anayankha Sauli, iye anati kwa ine, Undilole ndipite, ndingakuphe.