1 Samuel 19:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pompo adatumanso anthu kuti akamgwire. Anthuwo adaona gulu la aneneri akuvina namalosa, Samuele akuŵatsogolera. Pamenepo mzimu wa Mulungu udaŵaloŵa anthuwo ndipo nawonso adayamba kulosa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo anatumiza mithenga kuti igwire Davide, ndipo pamene inaona gulu la aneneri alikunenera, ndi Samuele mkulu wao alikuimapo, mzimu wa Mulungu unagwera mithenga ya Saulo, ninenera iyonso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho iye anatumiza anthu kuti akamugwire Davide. Koma anaona gulu la aneneri likulosera ndi Samueli akuwatsogolera. Pomwepo Mzimu wa Mulungu unawafikira ndipo nawonso anayamba kulosera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli anatumiza mithenga kuti igwire Davide, ndipo pamene inaona gulu la aneneri alikunenera, ndi Samueli mkuru wao alikuimapo, mzimu wa Mulungu unagwera-mithenga ya Sauli, ninenera iyonso.