1 Samuel 19:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nayenso adavula zovala zake namalosa pamaso pa Samuele, kenaka nkugona chamaliseche tsiku lonse, usana ndi usiku. Choncho padayambika chisudzo chakuti, “Kani Saulonso ali m'gulu la aneneri?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso anavula zovala zake, naneneranso pamaso pa Samuele, nagona wamaliseche usana womwe wonse, ndi usiku womwe wonse. Chifukwa chake amati, Kodi Saulonso ali pakati pa aneneri?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nayenso anavula zovala zake nayamba kulosa pamaso pa Samueli. Kenaka anagona wamaliseche tsiku lonse ndi usiku wonse. Nʼchifukwa chake anthu amati, “Kodi Sauli alinso mmodzi wa aneneri?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso anabvula zobvala zace, naneneranso pamaso pa Samueli nagona wamarisece usana womwe wonse, ndi usiku womwe wonse. Cifukwa cace amati, Kodi Saulinso ali pakati pa aneneri?