1 Samuel 19:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndidzapita ndi kukaima pakhundu pa bambo wanga kuminda kumene iwe ukabisaleko, tsono ndidzalankhula ndi bambo wanga za iwe. Chilichonse chimene ndidzamve, ndidzakuuza.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ine ndidzakutuluka ndi kuima pa mbali ya atate wanga kumunda kumene kuli iwe, ndipo ndidzalankhula ndi atate wanga za iwe; ndipo ndikaona kanthu ndidzakudziwitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndidzapita ndi kukayima pafupi ndi abambo anga ku munda kumene iwe ukabisale. Ndipo ndidzayankhula ndi abambo anga za iwe ndipo chilichonse chimene ndikamve ndidzakuwuza.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ine ndidzaturuka ndi kuima pa mbali ya atate wanga kumunda kumene kuli iwe, ndipo ndidzalankhula ndi atate wanga za iwe; ndipo ndikaona kanthu ndidzakudziwitsa.