1 Samuel 19:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yonatani adaterodi ndipo adakanena zabwino za Davide kwa bambo wake, namuuza kuti, “Atate, musachimwire mtumiki wanu Davide, poti sadakuchimwireni, koma amakuchitirani zabwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yonatani analankhula ndi Saulo atate wake movomereza Davide, nanena naye, Mfumu asachimwire mnyamata wake Davide; chifukwa iyeyo sanachimwire inu, ndipo ntchito zake anakuchitirani zinali zabwino ndithu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yonatani anakanena zabwino za Davide kwa abambo ake Sauli ndipo anati, “Mfumu musachimwire mtumiki wanu Davide, sanakuchimwireni, koma amakuchitirani zabwino kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Jonatani analankhula ndi atate wace mobvomereza Davide, nanena naye, Mfumu asacimwire mnyamata wace Davide; cifukwa iyeyo sanacimwira inu, ndipo nchito zace anakucitirani zinali zabwino ndithu;