1 Samuel 19:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja adaaika moyo wake pa minga pakupha Goliyati Mfilisti uja. Pambuyo pake Chauta adachita zazikulu pakupambanitsa Aisraele pa nkhondo. Inu mudaona zimenezo ndi kukondwera nazo. Chifukwa chiyani tsono mukufuna kuchimwira munthu wosalakwa, pofuna kumupha Davideyu?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza iye anataya moyo wake nakantha Mfilistiyo, ndipo Yehova anachitira Aisraele onse chipulumutso chachikulu, inu munachiona, nimunakondwera; tsono mudzachimwiranji mwazi wosalakwa, ndi kumupha Davide popanda chifukwa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayika moyo wake pa chiswe pamene anapha Mfilisiti uja. Choncho Yehova anachita zazikulu popambanitsa Aisraeli pa nkhondo. Inu munaona zonsezo ndipo munakondwera. Nanga nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchimwira munthu wosalakwa pofuna kupha Davide?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza iye anataya moyo wace nakantha Mfilistiyo, ndipo Yehova anacitira Aisrayeli onse cipulumutso cacikuru, inu munaciona, nimnnakondwera; tsono mudzacimwiranji mwazi wosalakwa, ndi kumupha Davide popanda cifukwa?