1 Samuel 2:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hana adapemphera nati, “Mtima wanga ukukondwa chifukwa cha zimene Chauta wandichitira, Ndikuyenda ndi mdidi chifukwa cha Chauta. Pakamwa panga pakula nkuseka adani anga monyodola. Ndakondwa kwambiri chifukwa mwandipulumutsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hana anapemphera, nati, Mtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova, nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova; pakamwa panga pakula kwa adani anga; popeza ndikondwera m'chipulumutso chanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Hana anapemphera nati, “Moyo wanga ukukondwera mwa Yehova; Ndiyenda mwa tukumutukumu chifukwa cha Yehova. Pakamwa panga pakula ndi kuseka adani anga mowanyogodola. Ndikukondwa chifukwa mwandipulumutsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hana anapemphera, nati Mtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova, Nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova; Pakamwa panga pakula kwa adani anga; Popeza ndikondwera m'cipulumutsocanu.