1 Samuel 2:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzatswanya adani ake, adzaŵaopsa ndi bingu kuchokera kumwamba. Chauta adzaŵaweruza mpaka ku mathero a dziko lapansi. Koma adzalimbikitsa mfumu yake, adzakuza mphamvu za wodzozedwa wake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika; kumwamba Iye adzagunda pa iwo; Yehova adzaweruza malekezero a dziko. Ndipo adzapatsa mphamvu mfumu yake, nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzaphwanya omutsutsa. Adzawaopsa ndi bingu kuchokera kumwamba; Yehova adzaweruza mathero a dziko lapansi. “Koma adzapereka mphamvu kwa mfumu yake, adzakuza mphamvu za odzozedwa wake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika; Kumwamba iye adzagunda pa iwo: Yehova adzaweruza malekezero a dziko: Ndipo adzapatsa mphamvu mfumuyace, Nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wace.