1 Samuel 2:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sankasamalanso za khalidwe loyenera ansembe pakati pa anthu. Ankachita motere: pamene munthu wina ankapereka nsembe, nyama ilikuŵira pa moto, mtumiki wake wa wansembe ankabwera, atatenga chiforoko cha mano atatu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo machitidwe a ansembe akuchitira anthu ndiwo, kuti pamene munthu aliyense akapereka nsembe, mnyamata wa wansembeyo akabwera, nyama ili chiwirire, ndi chovuulira cha ngowe cha mano atatu m'dzanja lake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo chizolowezi cha ansembe pakati pa anthu chinali motere kuti pamene munthu aliyense ankapereka nsembe ndipo nyama ija ikuwira pa moto, mtumiki wa wansembe ankabwera ndi chifoloko cha mano atatu mʼdzanja lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo macitidwe a ansembe akucitira anthu ndiwo, kuti pamene munthu ali yense akapereka nsembe, mnyamata wa wansembeyo akabwera, nyama iri ciwirire, ndi cobvuulira ca ngowe ca mana atatu m'dzanja lace;