1 Samuel 2:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuwonjezera apo, mafuta asanatenthedwe, mtumiki wa wansembe ankabwera ndi kuuza munthu wopereka nsembeyo kuti, “Patse nyama yoti ndikaotchere wansembe. Pakuti sadzalandira nyama yophika, koma yosaphika.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngakhale asanayambe kupsereza mafuta, amadza mnyamata wa wansembe, namuuza wopereka nsembe, nati, Umpatse wansembeyo nyama yoti akaotche; pakuti safuna nyama yako yophika koma yaiwisi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngakhale mafuta asanatenthedwe, mtumiki wansembe amabwera ndi kunena kwa munthu amene akupereka nsembeyo kuti, “Ndipatse nyama kuti ndiwotche, pakuti Yehova salandira nyama yophika koma yayiwisi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngakhale asanayambe kupsereza mafuta, amadza mnyamata wa wansembe, namuuza wopereka nsembe, nati, Umpatse wansembeyo nyama yoti akaoce; pakuti safuna nyama yako yophika koma yaiwisi.