1 Samuel 2:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo munthuyo akanena kuti, “Apserezeretu mafutaŵa poyamba, pambuyo pake ndiye mutenge monga momwe mufunira,” mtumiki uja ankati, “Iyai, patsiretu tsopano pompano. Ngati sutero, ndichita kukulanda.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ngati munthu akanena naye, Koma adzatentha mafuta tsopano apa, atatha, utenge monga mtima wako ufuna; uyo akanena naye, Iai, koma undipatsire iyo tsopanoli, ukapanda kutero ndidzailanda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati munthuyo anena kuti, “Apseretu mafuta poyamba, ndipo kenaka mutenge mmene mufunira,” mtumikiyo amayankha kuti, “Ayi ndipatse tsopano lino. Ngati sutero, ine nditenga molanda.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ngati munthu akanena naye, Koma adzatentha mafuta tsopano apa, atatha, utenge monga mtima wako ufuna; uyo akanena naye, lai, koma undipatsire iyo tsopanoli, ukapanda kutero ndidzailanda.