1 Samuel 2:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka chilichonse mai wake ankamsokera mkanjo, ndi kukampatsa pamene ankapita ndi mwamuna wake kukapereka nsembe ya chaka ndi chaka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso amake akamsokera mwinjiro waung'ono, nabwera nao kwa iye chaka ndi chaka, pakudza pamodzi ndi mwamuna wake kudzapereka nsembe ya pachaka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chaka chilichonse amayi ake ankamusokera kamkanjo ndi kukamupatsa akamapita ndi mwamuna wake kukapereka nsembe za pa chaka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso amace akamsokera mwinjiro waung'ono, nabwera nao kwa iye caka ndi caka, pakudza pamodzi ndi mwamuna wace kudzapereka nsembe ya pacaka.