1 Samuel 2:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Eli ankadalitsa Elikana ndi mkazi wake, ponena kuti, “Chauta akupatseni ana mwa mkazi ameneyu, chifukwa cha mwana amene iye adampereka kwa Chauta.” Atatero, iwowo ankabwerera kwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Eli anadalitsa Elikana ndi mkazi wake, nati, Yehova akupatse mbeu ndi mkazi uyu m'malo mwa iye amene munampempha kwa Yehova. Ndipo iwowa anabwera kwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Eli amadalitsa Elikana ndi mkazi wake ndi mawu akuti “Yehova akupatseni ana mwa mkazi uyu kulowa mʼmalo mwa amene anapempha ndi kumupereka kwa Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Eli anadalitsa Elikana ndi mkazi wace, nati, Yehova akupatse mbeu ndi mkazi uyu m'malo mwa iye amene munampempha kwa Yehova. Ndipo iwowa anabwera kwao.