1 Samuel 2:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano Eli adafika pokalamba kwambiri, ndipo ankamva zonse zimene ana ake aamuna ankachita Aisraele onse, ndiponso zoti anawo ankagona ndi akazi otumikira pa chipata cha chihema chamsonkhano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Eli anali wokalamba ndithu; namva zonse ana ake anachitira Aisraele onse, ndi kuti anagona ndi akazi akusonkhana pa khomo la chihema chokomanako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Eli anakalamba kwambiri. Iye ankamva zonse zimene ana ake aamuna ankachitira Aisraeli onse, ndiponso kuti ankagona ndi akazi pa chipata cha tenti ya msonkhano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Eli anali wokalamba ndithu; namva zonse ana ace anacitira Aisrayeli onse, ndi kuti anagona ndi akazi akusonkhana pa khomo la cihema cokomanako.