1 Samuel 2:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adafunsa ana akewo kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita zinthu zotere? Ndilikumvatu kwa anthu zonse zoipa zimene mukuchita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye ananena nao, Mumachitiranji chotere: popeza ndilinkumva za machitidwe anu oipa kwa anthu onsewa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukuchita zinthu zotere? Ine ndikumva kuchokera kwa anthu onse za zoyipa zanuzo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye ananena nao, Mumacitiranji zotere? popeza ndirinkumva za macitidwe anu oipa kwa anthu onsewa.