1 Samuel 2:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu akachimwira munthu mnzake, mwina Mulungu adzampepesera munthuyo. Koma akachimwira Chauta, adzampepesera ndani?” Koma anawo sadamvere mau a bambo wao, chifukwa kunali kufuna kwa Chauta kuti anawo aphedwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akachimwira munthu mnzake oweruza adzaweruza mlandu wake; koma ngati munthu achimwira Yehova, adzampembedzera ndani? Koma ngakhale adatero, iwo aja anakhalabe osamvera mau a atate wao, chifukwa Yehova adati adzawaononga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati munthu alakwira munthu mnzake, mwina Mulungu adzamupepesera, koma ngati munthu achimwira Yehova adzamupepesera ndani?” Koma ana ake sanamvere kudzudzula kwa abambo awo, pakuti chinali cholinga cha Yehova kuti awaphe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akacimwira munthu mnzace oweruza adzaweruza mrandu wace; koma ngati munthu acimwira Yehova, adzampembedzera ndani? Koma ngakhale adatero, iwo aja anakhalabe osamvera mau a atate wao, cifukwa Yehova adati adzawaononga.