1 Samuel 2:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina munthu wa Mulungu adafika kwa Eli namuuza kuti, “Chauta akuti, ‘Suja ndidadziwulula kwa banja la kholo lako Aroni pamene anali akapolo a Farao ku Ejipito?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anafika kwa Eli munthu wa Mulungu, nanena naye, Atero Yehova, Kodi Ine ndinadziwulula kwa banja la kholo lako, muja anali m'Ejipito, m'nyumba ya Farao?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina munthu wa Mulungu anabwera kwa Eli ndipo anamuwuza kuti, “Yehova akuti, ‘Kodi Ine sindinadziwulule ndekha kwa banja la kholo lako pamene iwo anali akapolo a Farao ku Igupto?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anafika kwa Eli munthu wa Mulungu, nanena naye, Atero Yehova, Kodi Ine ndinadziulula kwa banja la kholo lako, muja anali m'Aigupto, m'nyumba ya Farao?