1 Samuel 2:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ndidamsankha pakati pa mafuko onse a Israele, kuti akhale wansembe wanga, ndipo kuti azipita ku guwa langa lansembe, azifukiza lubani, ndi kumavala efodi pamaso panga. Ndidalipatsa banja la bambo wako gawo la nsembe zanga zonse zopsereza zimene Aisraele amapereka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi sindinasankhula iye pakati pa mafuko onse a Israele, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe pa guwa langa, nafukize zonunkhira, navale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatsa banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israele?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndinamusankha pakati pa mafuko a Israeli kuti akhale wansembe wanga ndi kuti azipita pa guwa langa la nsembe, kufukiza Lubani ndi kuvala efodi pamaso panga. Ndinapatsa banja la abambo ako gawo la nsembe zonse zopsereza zimene Aisraeli amapereka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi sindinasankhula iye pakati pa mafuko onse a Israyeli, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe pa guwa langa, nafukize zonunkhira, nabvale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatsa banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israyeli?