1 Samuel 2:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga chifukwa chiyani ukunyoza nsembe zanga ndi zopereka zanga zimene ndidalamula? Kodi ukulemekeza ana ako kupambana Ine, pomadzinenepetsa nonsenu ndi zakudya zokoma kwambiri za pa nsembe zanga zimene anthu anga Aisraele amapereka?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanga umaponderezeranji nsembe yanga ndi chopereka changa, zimene ndinalamulira m'mokhalamo mwanga; ndipo uchitira ana ako ulemu koposa Ine, kudzinenepetsa inu nokha ndi zokometsetsa za zopereka zao zonse za Aisraele, anthu anga?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chiyani ukunyoza nsembe ndi zopereka zanga zimene ndinalamula? Nʼchifukwa chiyani ukupereka ulemu kwa ana ako kuposa Ine podzinenepetsa nokha ndi zopereka zabwino kwambiri za nsembe zimene Aisraeli amapereka?’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanga umaponnderezeranji nsembe yanga ndi copereka canga, zimene ndinalamulira m'mokhalamo mwanga; ndipo ucitira ana ako ulemu koposa Ine, kudzinenepetsa inu nokha ndi zokometsetsa za zopereka zao zonse za Aisrayeli, anthu anga?