1 Samuel 2:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu inu musalankhulenso modzitama, pakamwa panu pasatuluke zodzikuza. Pakuti Chauta ndi Mulungu wanzeru, ndiye amene amaweruza ntchito za anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero; m'kamwa mwanu musatuluke zolulutsa; chifukwa Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo Iye ayesa zochita anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Musandiyankhulenso modzitama, pakamwa panu pasatuluke zonyada, pakuti Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo ndiye amene amayesa ntchito za anthu onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero; M'kamwa mwanu musaturuke zolulutsa; Cifukwa Yehova ali Mulungu wanzeru, Ndipo iye ayesa zocita anthu.