1 Samuel 2:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndidaalonjeza kuti anthu a pa banja lako ndi a pa banja la atate ako, azidzanditumikira nthaŵi zonse. Koma tsopano ndikuti zimenezo zithe basi! Ndidzachitira ulemu anthu ondichitira ulemu, koma anthu ondinyoza, Inenso ndidzaŵanyoza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Yehova Mulungu wa Israele akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Chikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Paja Ine Yehova Mulungu wa Israeli ‘Ndinalonjeza kuti anthu a pa banja lako ndi a pa banja la abambo ako azidzanditumikira nthawi zonse.’ Koma tsopano ndikuti, ‘Zonsezi zithe!’ Tsopano anthu amene amandilemekeza Inenso ndidzawalemekeza koma iwo amene amandinyoza Ine ndidzawanyoza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Yehova Mulungu wa Israyeli akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Cikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.