1 Samuel 2:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe pabanja pako ndidzasungapo mmodzi wodzanditumikira pa guwa langa, azidzangokuliritsa ndi kukumvetsa chisoni mumtima mwako. Koma ena onse a banja lako adzaphedwa ku nkhondo akali anyamata abiriŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu wako, amene ndidzamleka osamlikha pa guwa langa, adzatha maso ako, ndi kumvetsa mtima wako chisoni; ndipo obadwa onse a m'banja lako adzamwalira akali biriwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe pa banja lako mmodzi yekha ndidzamuleka wosamuchotsa kuti azidzanditumikira. Iyeyu azidzakuliritsa ndi kukumvetsa chisoni. Koma ena onse pa banja lako adzafa akanali aangʼono.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu wako, amene ndidzamleka osamlikha pa guwa langa, adzatha maso ako, ndi kumvetsa mtima wako cisoni; ndipo obadwa onse a m'banja lako adzamwalira akali biriwiri.