1 Samuel 2:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ndidzasankha wansembe wokhulupirika amene adzachita zinthu pomvera zimene mtima wanga ufuna ndiponso potsata maganizo anga. Ndidzammangira banja lolimba, ndipo adzatumikira pamaso pa wodzozedwa wanga nthaŵi zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzadziukitsira wansembe wokhulupirika, amene adzachita monga chimene chili mumtima mwanga ndi m'chifuniro changa; ndipo ndidzammangira nyumba yokhazikika, ndipo iyeyu adzayenda pamaso pa wodzozedwa wanga masiku onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake ndidzasankha wansembe wokhulupirika, amene adzachita zimene zili mu mtima ndi mʼmaganizo mwanga. Ndidzakhazikitsa banja lako kolimba ndipo adzatumikira pamaso pa wodzozedwa wanga nthawi zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzadziukitsira wansembe wokhulupirika, amene adzacita monga cimene ciri mumtima mwanga ndi m'cifuniro canga; ndipo ndidzammangira nyumba yokhazikika, ndipo iyeyu adzayenda pamaso pa wodzozedwa wanga masiku onse.