1 Samuel 2:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo aliyense amene adzatsale pabanja pako adzabwera kudzampempha iyeyo tindalama kapena kachakudya. Adzanena kuti, “Mundilole ndizithandizako ansembe, kuti ndipezeko kanthu kakudya.” ’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzali kuti yense wakusiyidwa wa m'banja lako adzabwera kwa iye nadzawerama ndi kupempha ndalama ndi chakudya, nadzati, Mundipatsetu ntchito ina ya wansembe, kuti ndikaona kakudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo aliyense wotsala wa banja lako adzabwera ndi kugwada pamaso pake kupempha ndalama kapena chakudya.’ Adzati, ‘Chonde ndiloleni kuti ndizithandizako pa ntchito iliyonse ya unsembe kuti ndipeze chakudya.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzali kuti yense wakusiyidwa wa m'banja lako adzabwera kwa iye nadzawerama ndi kupempha ndalama ndi cakudya, nadzati, Mundipatsetu nchito yina ya wansembe, kuti ndikaona kakudya.