1 Samuel 2:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amakweza osauka kuŵachotsa pa fumbi, amachotsa anthu osoŵa pa dzala, amaŵakhazika pamodzi ndi akalonga, amaŵapatsa mpando waulemu. Nsanamira za dziko lapansi nzake za Chauta, adakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amuutsa waumphawi m'fumbi, nanyamula wosowa padzala, kukamkhalitsa kwa akalonga; ndi kuti akhale nacho cholowa cha chimpando cha ulemerero. Chifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova, ndipo Iye anakhazika dziko pa izo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye amakweza osauka kuwachotsa pa fumbi, ndipo amachotsa anthu osowa pa dzala. Iye amawakhazika pamodzi ndi ana a mafumu, amawapatsa mpando waulemu. “Pakuti nsanamira za dziko lapansi ndi za Yehova, anakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amuutsa waumphawi m'pfumbi, Nanyamula wosowa padzala, Kukamkhalitsa kwa akalonga; Ndi kuti akhale naco colowa ca cimpando ca ulemerero; Cifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova, Ndipo iye anakhazika dziko pa izo,