1 Samuel 20:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adathaŵa ku Nayoti ku Rama, nabwera kwa Yonatani. Ndipo adafunsa Yonatani kuti, “Kodi ndidachita chiyani? Ndidalakwa chiyani? Kodi abambo ako ndidaŵachimwira chiyani, kuti azifuna kundipha?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anathawa ku Nayoti m'Rama, nadzanena pamaso pa Yonatani, Ndachitanji ine? Kuipa kwanga kuli kotani? Ndi tchimo langa la pamaso pa atate wanu ndi chiyani, kuti amafuna moyo wanga?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Davide anathawa ku Nayoti ku Rama ndi kupita kwa Yonatani ndipo anamufunsa kuti, “Kodi ine ndinachita chiyani? Kodi ndinalakwa chiyani? Kodi abambo ako ndinawalakwira chiyani kuti azifuna kundipha?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anathawa ku Nayoti m'Rama, nadzanena pamaso pa Jonatani, Ndacitanji ine? kuipa kwanga kuli kotani? ndi chimo langa la pamaso pa atate wanu ndi ciani, kuti amafuna moyo wanga?