1 Samuel 20:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumindako Yonatani adauza Davide kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akhale mboni. Nditaŵafunsa abambo anga nthaŵi yonga yomwe ino maŵa, ngakhale mkucha, ndipo ndikapeza kuti akufuna kukuchitira chinthu chabwino, ndidzatumiza mau kuti udziŵe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yonatani anati kwa Davide, Yehova, Mulungu wa Israele, akhale mboni; nditaphera mwambi atate wanga mawa dzuwa lino, kapena mkucha, onani, pakakhala kanthu kabwino kakuchitira Davide, sindidzakutumiza mthenga ndi kukuululira kodi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yonatani anawuza Davide kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akhale mboni! Ine ndikadzafunsa abambo anga nthawi yonga ino mmawa kapena mkuja, ndipo ndikadzapeza kuti akukufunira zabwino, ine ndidzatuma mawu kuti udziwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Jonatani anati kwa Davide, Yehova, Mulungu wa Israyeli, akhale mboni; nditaphera mwambi atate wanga mawa dzuwa lino, kapena mkuca, onani, pakakhala kanthu kabwino kakucitira Davide, sindidzakutumira mthenga ndi kukuululira kodi?