1 Samuel 20:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma akakafunitsitsa kukuchita choipa, Chauta adzandilange kwambiri ndikapanda kukuululira ndi kukuthandiza kuti upulumuke. Chauta akhale nawe, monga momwe adakhalira ndi abambo anga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulungu alange Yonatani, ndi kuonjezapo, ngati atate wanga akondwera kukuchitira choipa, ine osakuululira, ndi kukuchotsa kuti upite mumtendere; ndipo Yehova akhale nawe, monga anakhala naye atate wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati abambo anga atsimikiza kukuchita choyipa, Yehova andilange ine Yonatani, ndipotu kwambiri ngati sindidzakudziwitsa ndi kukulola kuti upite mu mtendere. Yehova akhale nawe monga anakhalira ndi abambo anga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu alange Jonatani, ndi kuonjezapo, ngati atate wanga akondwera kukucitira coipa, ine osakuululira, ndi kukucotsa kuti upite mumtendere; ndipo Yehova akhale nawe, monga anakhala naye atate wanga.