1 Samuel 20:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yonatani adatinso, “Maŵa mwezi ukhala, ndipo pa phwando adzazindikira kuti iwe palibe, popeza kuti pampando pako padzakhala popanda munthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono Yonatani ananena kwa Davide, Mawa mwezi ukhala; ndipo adzakufuna, popeza udzasoweka pamalo pako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yonatani anawuzanso Davide kuti, “Mawa ndi tsiku la chikondwerero cha mwezi watsopano. Zidzadziwika kuti iwe palibe chifukwa mpando wako udzakhala wopanda munthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono Jonatani ananena kwa Davide, Mawa mwezi ukhala; ndipo adzakufuna, popeza udzasoweka pamalo pako.