1 Samuel 20:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndidzatuma mnyamata wanga kuti akatole miviyo. Mnyamatayo ndikamuuza kuti, ‘Mivi ili chakuno, kaitole!’ Pomwepo iweyo udzatuluke, chifukwa ndikulumbira, pali Chauta wamoyo, kuti kuli mtendere, iwe sudzakhala pa zoopsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo taona, ndidzatumiza mnyamatayo, ndi kuti, Kafune miviyo. Ndikamuuza mwanayo, kuti, Taona mivi ili chakuno; uitole nubwere, popeza pali mtendere kwa iwe, palibe kanthu, pali Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndidzatuma mnyamata ndi kuti, ‘Pita ukatole miviyo!’ Ngati ndidzanena kwa iye kuti, ‘Taona, mivi ili mbali yakuno, kayitole,’ iwe ukatuluke, pakuti ndikulumbira, pali Yehova Wamoyo, ndiye kuti zako zili bwino, palibe choopsa chilichonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo taona, ndidzatumiza mnyamatayo, ndi kuti, Kafune mibviyo, Ndikamuuza mwanayo, kuti, Taona mibvi iri cakuno; uitole nubwere, popeza pali mtendere kwa iwe, palibe kanthu, pali Yehova.