1 Samuel 20:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adakhala pa mpando wake pafupi ndi khoma, monga m'mene ankachitira nthaŵi zonse. Yonatani adakhala popenyana naye, ndipo Abinere adakhala pambali pa mfumu Saulo, koma pa malo a Davide panalibe munthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mfumu nikhala pa mpando wake, monga ankachita nthawi zina, pa mpando wa pafupi pa khoma. Ndipo Yonatani anaimirira, ndi Abinere anakhala pa mbali ya Saulo; koma Davide anasoweka pamalo pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anakhala pa malo ake a nthawi zonse pafupi ndi khoma moyangʼanana ndi Yonatani, ndipo Abineri anakhala moyandikana ndi Sauli, koma pa malo a Davide panalibe munthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mfumu nikhala pa mpando wace, monga adafocita nthawi zina, pa mpando wa pafupi pa khoma. Ndipo Jonatani anaimirira, ndi Abineri anakhala pa mbali ya Sauli; koma Davide anasoweka pamalo pace.