1 Samuel 20:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Saulo sadanene kanthu kalikonse tsiku limenelo. Ankaganiza kuti, “Chinthu china chamgwera Davide, mwina mwake ngwosayenera zachipembedzo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Saulo sananene kanthu tsiku lomwelo; chifukwa anaganizira, Kanthu kanamgwera iye, ali wodetsedwa; indedi ali wodetsedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli sananene chilichonse tsiku limenelo pakuti ankaganiza kuti “Chilipo chimene chachitika ndi Davide. Mwina mwake ngosayenera za chipembedzo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Sauli sananena kanthu tsiku lomwelo; cifukwa anaganizira, Kanthu kanamgwera iye, ali wodetsedwa; indedi ali wodetsedwa.