1 Samuel 20:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pa tsiku lachiŵiri la phwandolo, pa malo a Davide panalibenso munthu. Ndiye Saulo adafunsa Yonatani kuti, “Chifukwa chiyani Davide mwana wa Yese sadabwere ku phwando dzulo ngakhalenso lero?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali tsiku lachiwiri mwezi utakhala, Davide adasowekanso pamalo pake; ndipo Saulo anati kwa Yonatani mwana wake, Mwana wa Yese walekeranji kubwera kudya dzulo ndi lero lomwe?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pa tsiku lachiwiri la chikondwerero cha mwezi watsopano pamalo pa Davide panalibenso munthu. Kenaka Sauli anafunsa Yonatani kuti, “Nʼchifukwa chiyani mwana wa Yese sanabwere kudzadya, dzulo ngakhale lero?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali tsiku laciwiri mwezi utakhala, Davide adasowekanso pamalo pace; ndipo Sauli anati kwa Jonatani mwana wace, Mwana wa Jese walekeranji kubwera kudya dzulo ndi lero lomwe?