1 Samuel 20:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adati, ‘Undilole ndipite, popeza kuti banja lathu likupereka nsembe mumzindamo, ndipo mbale wanga adandikakamiza kuti ndikakhale nao kumeneko. Tsono ngati wandikomera mtima, undilole ndipite, kuti ndikaone abale anga.’ Nchifukwa chake sadabwere ku chakudya cha mfumu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nati, Ndiloleni, ndimuke; chifukwa banja lathu lipereka nsembe m'mudzimo; ndi mbale wanga anandiuzitsa ndifikeko; tsono ngati wandikomera mtima undilole ndichoke, ndikaone abale anga. Chifukwa cha ichi safika ku gome la mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anati, ‘Undilole ndipite, chifukwa banja lathu likupereka nsembe mu mzindamo ndipo mʼbale wanga wandiwumiriza kuti ndikakhale nawo. Ngati wandikomera mtima, chonde ndilole ndipite ndikaone abale anga.’ Nʼchifukwa chake sanabwere kudzadya ndi mfumu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nati, Ndiloleni, ndimuke; cifukwa banja lathu lipereka nsembe m'mudzimo; ndi mbale wanga anandiuzitsa ndifikeko; tsono ngati wandikomera mtima undilole ndicoke, ndikaone abale anga. Cifukwa ca ici safika ku gome la mfumu.