1 Samuel 20:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Davide adalumbira kuti, “Abambo ako akudziŵa bwino lomwe kuti umandikonda, ndipo adati, ‘Yonatani asadziŵe zimenezi kuwopa kuti angamve chisoni.’ Koma ndithu, Mulungudi, iwe Yonatani uli apa, imfa sili nane kutali.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Davide analumbira kuti, “Abambo ako akudziwa bwino lomwe kuti iwe umandikonda ndipo iwo amaganiza kuti, Yonatani sayenera kudziwa zimenezi mwina adzamva chisoni kwambiri. Komabe, pali Yehova ndi pali iwe, imfa sinanditalikire.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Jonatani asadziwe ici, kuti angamve cisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazilimodzi.