1 Samuel 20:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Saulo adapsera mtima Yonatani kwambiri, ndipo adamuuza kuti, “Iwe mwana wobadwa kwa chimkazi chapakamwa, kodi ukuyesa kuti sindikudziŵa ine kuti ukugwirizana ndi mwana wa Yese, amene afuna kukuchititsa manyazi iwe ndi mai wakoyo?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Saulo anapsa mtima ndi Yonatani, nanena naye, Iwe mwana wa mkazi wa matsutso ndi wopikisana, sindidziwa kodi kuti wasankha mwana wa Yeseyo kudzinyaza wekha, ndi usiwa wa mai wako yemwe?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli anamupsera mtima Yonatani ndipo namuwuza kuti, “Iwe mwana wobadwa mwa mkazi wamakhalidwe oyipa ndi wowukira! Kodi ukuyesa kuti ine sindikudziwa kuti umagwirizana ndi mwana wa Yese, amene akufuna kukuchititsa manyazi iwe ndi amayi ako?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Sauli anapsa mtima ndi Jonatani, nanena naye, Iwe mwana wa mkazi wa matsutso ndi wopikisana, sindidziwa kodi kuti wasankha mwana wa Jeseyo kudzinyaza wekha, ndi usiwa wa mai wako yemwe?