1 Samuel 20:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi sukudziŵa kuti mwana wa Yese akakhalabe ndi moyo pa dziko lapansi, iweyo sudzakhala mfumu? Nchifukwa chake tsono, tuma anthu kuti akamtenge, abwere naye kuno, pakuti ndithudi adzafa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza nthawi yonse mwana wa Yeseyo akhala ndi moyo padziko, koma sudzakhazikika iwe, kapena ufumu wako. Chifukwa chake tumiza tsopano numtengere kuno kwa ine, popeza adzafa ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana wa Yese akakhala ndi moyo pa dziko lapansi lino, iwe sudzakhala mfumu. Tsopano tumiza munthu akamutenge kubwera naye kwa ine, pakuti Davide ayenera kufa basi!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza nthawi yonse mwana wa Jeseyo akhala ndi moyo padziko, koma sudzakhazikika iwe, kapena ufumu wako. Cifukwa cace tumiza tsopano numtengere kuno kwa ine, popeza adzafa ndithu,