1 Samuel 20:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yonatani adanyamuka pa tebulo atakwiya koopsa, ndipo pa tsiku lachiŵiri la phwandolo sadadye. Adaavutika kwambiri mumtima mwake, chifukwa choti bambo wake adaachita Davide chipongwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Yonatani anauka pagome wolunda ndithu, osadya kanthu tsiku lachiwiri la mwezi, pakuti mtima wake unali ndi chisoni chifukwa cha Davide, popeza atate wake anamchititsa manyazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yonatani anachoka pa tebulopo ali wopsa mtima kwambiri. Tsiku lachiwiri la chikondwererocho Yonatani sanadye chakudya. Iye anawawidwa mtima chifukwa abambo ake anatsimikiza zakupha Davide.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Jonatani anauka pagome wolunda ndithu, osadya kanthu tsiku laciwiri la mwezi, pakuti mtima wace unali ndi cisoni cifukwa ca Davide, popeza atate wace anamcititsa manyazi.