1 Samuel 20:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adauza mnyamata wake kuti, “Thamanga, ukatole mivi imene nditi ndiponye.” Mnyamata uja akuthamanga, Yonatani adaponya muvi patsogolo pa mnyamatayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anauza mnyamata wakeyo, Thamanga uzikatola mivi imene ndidzaponya; ndipo analikuthamanga mnyamatayu, iye anaponya muvi kuutumphitsa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anawuza mnyamatayo kuti, “Thamanga ukatole muvi umene nditi ndiponye.” Mnyamatayo akuthamanga Yonatani anaponya muvi patsogolo pa mnyamatayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anauza mnyamata waceyo, Thamanga uzikatola mibvi Imene ndidzaponya; ndipo analikuthamanga mnyamatayu, iye anaponya mubvi kuutumphitsa iye.