1 Samuel 20:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo mnyamatayo atafika pamalo pomwe padaagwa muviwo, Yonatani adanena chokweza kuti, “Muvi uli patsogolo pakopo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mnyamatayo atafika pa malo a muvi umene Yonatani anauponya, nati, Muviwo suli m'tsogolo mwako kodi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mnyamatayo atafika pamene muvi wa Yonatani unagwera,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mnyamatayo atafika pa malo a mubvi umene Jonatani anauponya, Jonatani anapfuulira mnyamatayo, nati, Mubviwo suli m'tsogolo mwako kodi?