1 Samuel 20:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Yonatani adaitananso mnyamatayo nati, “Fulumira, yenda msanga, usachedwe.” Motero mnyamata uja adatola muviwo, nabwera kwa mbuyake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yonatani anafuulira mnyamatayo, nati, Yendetsa, fulumira, usaima. Ndi mnyamata wa Yonatani anatola mivi, nafika kwa mbuye wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yonatani anayitananso mnyamatayo kuti, “Fulumira, pita msanga usayime.” Choncho mnyamatayo anatola muvi uja ndi kubwera nayo kwa mbuye wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Jonatani anapfuulira mnyamatayo, nati, Yendesa, fulumira, usaima. Ndi mnyamata wa Jonatani anatola mibvi, nafika kwa mbuye wace.