1 Samuel 20:41 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mnyamatayo atapita, Davide adatulukira ku mbali ina ya mulu wa miyala uja, ndipo adadzigwetsa pansi nagunditsa nkhope yake pansi katatu. Adampsompsonana, nayamba kulira onse aŵiriwo, koma Davide adalira koposa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo pochoka mnyamatayo, Davide, anauka chakumwera, nagwa nkhope yake pansi, nawerama katatu; ndipo iwowa anapsompsonana, nalirirana, kufikira Davide analiritsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mnyamatayo anapita. Kenaka Davide anatuluka ku mbali ina ya mulu wa miyala uja, nadzigwetsa pansi ndi kugunditsa nkhope yake pansi katatu. Anapsompsona nayamba kulira onse awiri, koma Davide analira kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo pocoka mnyamatayo, Davide anauka cakumwera, nagwa nkhope yace pansi, nawerama katatu; ndipo iwowa anapsompsonana, nalirirana, kufikira Davide analiritsa.