1 Samuel 20:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adati, “Paja maŵa kuli phwando la mwezi wokhala chatsopano, ndipo sindiyenera kulephera kukadya ndi mfumu. Koma undilole ndipite kuti ndikabisale ku thengo mpaka mkucha madzulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Davide kwa Yonatani, Onani, mawa mwezi ukhala, ndipo ine ndiyenera kupita kukadya kwa mfumu, wosatsala; koma undilole ndikabisale kuthengo, kufikira tsiku lachitatu madzulo ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Davide anati, “Taona mawa ndi tsiku la chikondwerero cha mwezi watsopano, ndipo ine ndiyenera kukadya ndi mfumu. Koma undilole ndipite ndikabisale mʼmunda mpaka mkuja madzulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Davide kwa Jonatani, Onani, mawa mwezi ukhala, ndipo ine ndiyenera kupita kukadya kwa mfumu, wosatsala; koma undilole ndikabisale kuthengo, kufikira tsiku lacitatu madzulo ace.