1 Samuel 20:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abambo ako akandifuna, uŵauze kuti, ‘Davide adandiwumiriza kuti ndimlole kuti athamangire ku mzinda wakwao ku Betelehemu. Akuti kumeneko kuli nsembe yapachaka ya banja lonse.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atate wako akandifuna pang'ono ponse, unene kuti, Davide anandiumirira ndimlole athamangire kwao ku Betelehemu, pakuti kumeneko kuli nsembe ya pachaka ya banja lao lonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati abambo ako akafunsa za ine, ukawawuze kuti, ‘Davide anandiwumiriza kuti ndimulole apite msanga kwawo ku Betelehemu, chifukwa akupereka nsembe yapachaka ya banja lonse.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atate wako akandifuna pang'ono ponse, unene kuti, Davide anandiumirira ndimlole athamangire kwao ku Betelehemu, pakuti kumeneko kuli nsembe ya pacaka ya banja lao lonse.