1 Samuel 20:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake undikomere mtima, poti udachita chipangano ndi ine kapolo wako pamaso pa Chauta. Koma ngati ndalakwa, undiphe ndiwe osati ukanditule kwa abambo ako.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake uchitire kapolo wako zokoma mtima; popeza wamchititsa kapolo wako kupangana nawe pangano la kwa Yehova; koma ngati mwa ine muli choipa chilichonse, undiphe wekha; udzapita nane bwanji kwa atate wako?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma undikomere mtima ine mtumiki wako, pakuti unapangana nane pangano pamaso pa Yehova. Ngati ndine wolakwa undiphe ndiwe, koma usandipereke kwa abambo ako.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ucitire kapolo wako zokoma mtima; popeza wamcititsa kapolo wako kupangana nawe pangano la kwa Yehova; koma ngati mwa ine muli coipa ciri conse, undiphe wekha; udzapita nane bwanji kwa atate wako?