1 Samuel 21:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adakafika ku Nobu kwa wansembe Ahimeleki. Ahimelekiyo adadzamchingamira akunjenjemera, namufunsa kuti, “Zatani kuti muli nokha popanda ndi mmodzi yemwe wokuperekezani?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anafika ku Nobu kwa Ahimeleki wansembeyo; ndipo Ahimeleki anadza kukomana ndi Davide alikunjenjemera, nanena naye, Muli nokha bwanji, palibe munthu wina nanu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anapita ku Nobi kwa wansembe Ahimeleki. Ahimelekiyo ankanjenjemera pamene ankamuchingamira, ndipo anafunsa kuti, “Muli nokha chifukwa chiyani? Chifukwa chiyani mulibe wokuperekezani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anafika ku Nobi kwa! Ahimeleki wansembeyo; ndipo Ahimeleki anadza kukomana ndi Davide alikunjenjemera, nanena naye, Muli nokha bwanji, palibe munthu wina nanu?