1 Samuel 21:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho adasintha khalidwe lake pamaso pao, nadzisandutsa ngati wamisala, namangolembalemba pa zitseko za chipata, malovu ali chuchuchu kutsikira ku ndevu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nasanduliza makhalidwe ake pamaso pao, nadzionetsera m'manja mwao ngati wamisala, nangolembalemba pa zitseko za chipata, nakhetsa dovu lake pa ndevu yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anasintha makhalidwe ake pamaso pawo, nʼkudzisandutsa ngati wamisala. Iye ankangolembalemba pa zitseko za chipata ndi kumangotuluka dovi, nʼkumayenderera mʼndevu zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nasanduliza makhalidwe ace pamaso pao, nadzionetsera m'manja mwao ngati wamisala, nangolembalemba pa zitseko za cipata, nakhetsa dobvu lace pa ndebvu yace.