1 Samuel 21:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adayankha kuti, “Mfumu yandituma ndipo yandilamula kuti ndisauze munthu wina aliyense zimene yanditumazo. Kunena za anthu anga, ndapangana nawo kuti tikakumane pa malo ena ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Davide kwa Ahimeleki wansembeyo, Mfumu inandilamulira ntchito, ninena nane, Asadziwe munthu aliyense kanthu za ntchito imene ndakutumira ndi kukulamulira; ndipo ndawapanga anyamatawo ku malo akuti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anayankha Ahimeleki kuti, “Mfumu yandituma zinthu zina ndipo yandiwuza kuti, ‘Munthu aliyense asadziwe za zimene ndakutumazo.’ Kunena za anthu anga, ndawawuza kuti tikakumane pamalo pena pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Davide kwa Ahimeleki wansembeyo, Mfumu inandilamulira nchito, ninena nane, Asadziwe munthu ali yense kanthu za nchito imene ndakutumira ndi kukulamulira; ndipo ndawapanga anyamatawo ku malo akuti.