1 Samuel 21:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wansembeyo adayankha kuti, “Pano ndilibe buledi wamba, koma alipo ndi buledi wachipembedzo. Ngati anthu anu sadakhale ndi akazi ao, angathe kudya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembeyo anayankha Davide nati, Ndilibe mkate wachabe, koma ulipo mkate wopatulika; pokhapo ngati anyamatawo anadzisunga kupewa akazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma wansembeyo anamuyankha Davide kuti, “Ine ndilibe buledi wamba woti ndikupatseni. Koma pali buledi wachipembedzo yekha. Ngati anthu amene muli nawo sanagone ndi akazi awo mukhoza kudya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembeyo anayankha Davide nati, Ndiribe mkate wacabe, koma ulipo mkate wopatulika; pokhapo ngati anyamatawo anadzisunga kupewa akazi.