1 Samuel 21:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adayankha kuti, “Kunena zoona, nthaŵi zonse tikakhala pa ulendo, timakhala odzimanga. Anthu anga amakhala odzimanga ngakhale pa ulendo wamba, nanji lero pamene tili pa ulendo woterewu!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anayankha wansembeyo, nati naye, Zoonadi tinafulatira akazi monga masiku atatu; chichokere ine, zotengera za anyamatawo zinali zopatulika ungakhale unali ulendo wachabe; koposa kotani nanga zotengera zao zikhala zoyera lero?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anayankha kuti, “Kunena zoona sitinakhudzane ndi mkazi monga timachitira nthawi zonse tikakhala pa ulendo. Anthu anga salola kudziyipitsa ndi mkazi ngakhale pa ulendo wamba. Nanji lero tili pa ulendo woterewu!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anayankha wansembeyo, nati naye, Zoonadi tinafulatira akazi monga masiku atatu; cicokere ine, zotengera za anayamatawo zinali zopatulika ungakhale unali ulendo wacabe; koposa kotani nanga zotengera zao zikhala zoyera lero?